Psalms 129

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,”
anene tsono Israeli;
2“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,
koma sanandipambane.
3Anthu otipula analima pa msana panga
ndipo anapangapo mizere yayitali:
4Koma Yehova ndi wolungama;
Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”

5Onse amene amadana ndi Ziyoni
abwezedwe pambuyo mwamanyazi.
6Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,
umene umafota usanakule;
7sungadzaze manja a owumweta
kapena manja a omanga mitolo.
8Odutsa pafupi asanene kuti,
“Dalitso la Yehova lili pa inu;
tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”
Copyright information for NyaCCL